Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 24

Yang’ananibe Pamphotho!

Yang’ananibe Pamphotho!

(2 Akorinto 4:18)

1. Pomwe akhungu adzaona

Ndipo ogontha adzamvanso,

Pamene madzi adzayenda

Ngakhale muchipululu,

Pomwe wolumala ’dzadumpha,

Abale athu sadzafanso,

Mudzaona madalitsowa

M’kayang’anabe pamphotho.

2. Osalankhula ’dzalankhula,

Okalamba ku unyamata,

Pomwe nthaka idzatulutsa

Zinthu zambiri zabwino,

Pomwe ana ’dzaimba nyimbo,

Kudzakhala mtendere konse,

M’dzaona ’kufa atauka,

M’kayang’anabe pamphotho.

3. Mimbulu idzadya ndi nkhosa,

Zilombo zoopsa ndi ng’ombe.

Mwana adzazitsogolera,

Ndipo zidzamvera iye.

Pamene mantha ndi misozi

Zidzakhala zinthu zakale,

Mudzaona zinthu zonsezi,

M’kayang’anabe pamphotho.

(Onaninso Yes. 11:6-9; 35:5-7; Yoh. 11:24.)