Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 28

Nyimbo Yatsopano

Nyimbo Yatsopano

(Salmo 98)

1. Imbira M’lungu, Imba nyimbo yatsopano;

Unene kwa onse Ntchito zake zonse.

Umutamande, Mulungu ndi wopambana.

Poweruza anthu N’ngwachilungamodi.

(KOLASI)

Imbani!

Nyimbo yatsopano!

Imbani!

Yehova ndi Mfumu.

2. Fu’la mokondwa, Fuula kwa Mfumu yathu!

Mutamandenitu, Ndi nyimbo mokondwa.

Tiyeni tonse Timuimbire mokweza.

Zeze ndi lipenga Ziimbe pamodzi.

(KOLASI)

Imbani!

Nyimbo yatsopano!

Imbani!

Yehova ndi Mfumu.

3. Nyanja ndi zinthu Za momwemo zim’tamande.

Inde chilengedwe Chonse chim’tamande.

Mtunda ukondwe, Mitsinjenso ikondwere.

Mapiri ndi zigwa, Nazo zim’tamande.

(KOLASI)

Imbani!

Nyimbo yatsopano!

Imbani!

Yehova ndi Mfumu.

(Onaninso Sal. 96:1; 149:1; Yes. 42:10.)