Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 37

Malemba Anauziridwa ndi Mulungu

Malemba Anauziridwa ndi Mulungu

(2 Timoteyo 3:16, 17)

1. M’dzikoli, Mawu a M’lungu

Amatiunikira.

Tikawatsatira bwino,

Cho’nadi chitimasula.

2. Mawu ndi ouziridwa,

Amatiphunzitsadi.

Amawongoladi zinthu

Ndiponso kutilangiza.

3. Malemba akumwambawa,

Atidziwitsa M’lungu.

Ngati timawawerenga,

Tingadzapezedi mphoto.

(Onaninso Sal. 119:105; Miy. 4:13.)