Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 29

Yendani ndi Mtima Wosagawanika

Yendani ndi Mtima Wosagawanika

(Salmo 26)

1. Mundiweruzetu Mbuye wanga;

Onani kuti ndimakudalirani.

Ndisanthuleni ndi kundiyesa;

Konzani mtima wanga, mundidalitse.

(KOLASI)

Koma ine, Ndatsimikizadi

Kusonyeza mtima Wosagawanika

2. Sindikhala pa anthu achabe.

Ndidana ndi anthu onyoza cho’nadi.

Musandichotsetu ndi ochimwa

Kapena ndi anthu okonda ziphuphu.

(KOLASI)

Koma ine, Ndatsimikizadi

Kusonyeza mtima Wosagawanika

3. Ndikonda kukhala m’nyumba yanu.

Ndidzachirikiza kulambira kwanu.

Ndidzayendadi kuguwa lanu,

Pokuyamikani mokweza kwambiri.

(KOLASI)

Koma ine, Ndatsimikizadi

Kusonyeza mtima Wosagawanika

(Onaninso Sal. 25:2.)