Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 2

Tikuyamikani Yehova

Tikuyamikani Yehova

(1 Atesalonika 5:18)

1. Tikuyamikani Yehova M’lungu,

Mumatipatsa kuwala kwanu.

Tikuyamika mwayi wa pemphero,

Kuti tinene mavuto athu.

2. Tikuyamika potumiza Yesu

Amene anagonjetsa dziko.

Tikuyamikani potithandiza

Kukwaniritsa lonjezo lathu.

3. Tikuyamika chifukwa cha mwayi

Wolalikira za dzina lanu.

Tiyamika mudzathetsa mavuto,

Madalitso anu sadzathadi.

(Onaninso Sal. 50:14; 95:2; 147:7; Akol. 3:15.)