Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 30

Ufumu wa Yehova Wayamba Kulamulira

Ufumu wa Yehova Wayamba Kulamulira

(Chivumbulutso 11:15)

1. Tsikuli n’lapadera. M’lungu akulamula.

Waikatu mwala mu Ziyoni.

Onse akweze mawu. Aimbire Mulungu.

Khristu Mpulumutsi wakhala pampando.

(KOLASI)

Kodi Ufumu wa Yehova

Udzabweretsa chiyani?

Udzadzetsa moyo wosatha

Ndi chimwemwe chochuluka.

Tamanda Mfumu yosatha

Iye ndi wachifundo.

2. Khristu ali pampando, Nkhondo yayandikira.

Dongosolo la Satana litha.

Ndi nthawi yolalika kwa anthu ochuluka.

Nyengo yoti ofatsa asankhe M’lungu.

(KOLASI)

Kodi Ufumu wa Yehova

Udzabweretsa chiyani?

Udzadzetsa moyo wosatha

Ndi chimwemwe chochuluka.

Tamanda Mfumu yosatha

Iye ndi wachifundo.

3. Tidalira Mfumuyo. Ndi yochititsa chidwi.

Ibwera mu dzina la Yehova.

Tilowe mukachisi, Tim’pembedze Mulungu.

Posachedwa adzalamulira zonse.

(KOLASI)

Kodi Ufumu wa Yehova

Udzabweretsa chiyani?

Udzadzetsa moyo wosatha

Ndi chimwemwe chochuluka.

Tamanda Mfumu yosatha

Iye ndi wachifundo.

(Onaninso 2 Sam. 7:22; Dan. 2:44; Chiv. 7:15.)