Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 32

Khalani Olimba, Osasunthika

Khalani Olimba, Osasunthika

(1 Akorinto 15:58)

1. Anthu akuvutika kwambiri.

Poopa zinthu zili m’tsogolo.

Tikhale osasunthika konse,

Potumikira M’lungu.

(KOLASI)

Tikhaletu olimba

Tisiyane ndi dziko.

Tidye choonadi,tikhulupirike.

2. Misampha ndi yambiri m’dzikoli.

Koma mwanzeru tingaipewe.

Tikakhulupirira Mulungu,

Adzatisamalira.

(KOLASI)

Tikhaletu olimba

Tisiyane ndi dziko.

Tidye choonadi,tikhulupirike.

3. Tilambire Yehova Mulungu,

Tim’tumikire mogwirizana.

Tilalike uthenga mwachangu,

Mapeto adzafika.

(KOLASI)

Tikhaletu olimba

Tisiyane ndi dziko.

Tidye choonadi,tikhulupirike.

(Onaninso Luka 21:9; 1 Pet. 4:7.)