Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 35

Tikuthokoza Mulungu Chifukwa cha Kuleza Mtima Kwake

Tikuthokoza Mulungu Chifukwa cha Kuleza Mtima Kwake

(2 Petulo 3:15)

1. Yehova, Mulungu wamphamvu,

Mumakondatu zabwino.

Zoipa n’zambiri m’dziko,

Ndipo zimakuwawani.

Tidziwa simuzengereza,

Mudzathetsadi zoipazi.

Tiyembekeza pa inu.

Choncho tikukuthokozani.

2. Zaka chikwi zilitu ngati

Tsiku limodzi kwa inu.

Tsiku lanu layandika,

Ndipo silichedwa konse.

Anthu ochimwa akalapa

Mtima wanu usangalala.

Tikukuthokozanitu,

Tiyembekezera pa inu.

(Onaninso Luka 15:7; 2 Pet. 3:8, 9.)