Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 6

Pemphero la Mtumiki wa Mulungu

Pemphero la Mtumiki wa Mulungu

(Aefeso 6:18)

1. Atate wa kumwamba, Mfumu,

Dzina lanu litamandidwetu

Chifundo chanu ndi chosatha,

Komanso ndi chodalirika.

Inde n’chodalirika,

Chifundochi n’chosatha.

2. Mtima wathu uthandizeni

Kuti uzikonda choonadi.

Malamulo anu tisunge,

Nkhosa zanuzo tizifune.

Nkhosa zanu tifune,

Malamulo tisunge.

3. M’tipatse nzeru yakumwamba,

M’tidzaze ndi chikondi mumtima

M’tithandize kukonda anthu,

Onse adziwe M’lungu wathu.

Inde akudziweni,

Tiwakondedi anthu.

(Onaninso Sal. 143:10; Yoh. 21:15-17; Yak. 1:5.)