Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 39

Mtendere Wathu Wamtengo Wapatali

Mtendere Wathu Wamtengo Wapatali

(Yohane 14:27)

1. Tamandani Yehova

Wamtendereyo.

Nkhondo adzazithetsa

Mwa Mwana wake,

Ndipo adzapambana

Nkhondo yabwino

N’kubweretsa mtendere

Padziko lonse.

2. Ukali ndi mkangano,

Izi tasiya.

Mikondo ndi lupanga

Zonse tataya.

Tilitu pa mtendere

Ndi anthu onse.

Monga nkhosa za Yesu,

Ee, zamtendere.

3. Mtendere ndi chipatso

Chachilungamo,

Ndi nzeru yakumwamba,

Yomwe tipempha.

Tiyendebe m’njirayi,

Timaikonda,

Mtendere udzakhala

Padziko lonse.

(Onaninso Sal. 46:9; Yes. 2:4; Yak. 1:17, 18.)