Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 83

Tifunika Kukhala Odziletsa

Tifunika Kukhala Odziletsa

(Aroma 7:14-25)

1. Timakonda Yehova kwambiri

Koma ndife anthu ochimwa zedi

Choterotu ndi kofunika

Kuti tikhale odziletsa.

2. Satana ndi matupi ochimwa

Tsiku lililonse amatiyesa.

Koma tikadalira M’lungu

Adzateteza mtima wathu.

3. Tanyamula dzina la Yehova

Choncho tisapezeredwe chifukwa.

Pa chilichonse timachita

Tikhale anthu odziletsa.

(Onaninso 1 Akor. 9:25; Agal. 5:23; 2 Pet. 1:6.)