Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 87

Tsopano Ndife Thupi Limodzi

Tsopano Ndife Thupi Limodzi

(Genesis 2:23, 24)

1. Fupa la mafupa anga,

Ndiwe mnofu wa mnofu wanga.

M’lungu wandipatsa mnzanga,

Inde wangawanga.

Tsopano tili amodzi,

Yehova ankafuna chonchi.

Monga mwamuna ndi mkazi,

Banja n’limeneli.

Mulungu atitsogolera.

Tsiku ndi tsiku

Chikondi tisonyeza.

Mmene talonjezerana

Zichitike, tizikondana.

Tilemekeze Yehova,

Ndipo ukhalebe wanga.

(Onaninso Gen. 29:18; Mlal. 4:9, 10; 1 Akor. 13:8.)