Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 47

Lalikirani Uthenga Wabwino

Lalikirani Uthenga Wabwino

(Chivumbulutso 14:6, 7)

1. Poyamba sitinkadziwa za Ufumu.

Pano tikudziwa Mbewu yalonjezo.

Mwa chifundo ndi chikondi cha Yehova,

Anaganizira anthu ochimwafe.

Anakonza zoti Yesu alamule.

Ufumuwo unali woti udzabadwe.

Komanso kusankha kagulu ka nkhosa

Kadzakhale mkwatibwi wa Mwana wake.

2. Mulungu ankadziwa za uthengawu.

Tsopano afuna anthu audziwe.

Angelo amakondwa potithandiza

Kuchita ntchito yolengeza Ufumu.

Tilitu ndi udindo ndiponso mwayi

Wom’tamanda ndi kuyeretsa dzina lake.

Tili ndi mwayi wolengeza dzinalo

Mwa kulalikira uthenga wabwino.

(Onaninso Maliko 4:11; Mac. 5:31; 1 Akor. 2:1, 7.)