Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 49

Yehova Ndi Pothawira Pathu

Yehova Ndi Pothawira Pathu

(Salmo 91)

1. Yehova m’pothawira

Tidalira iye.

Tikhalebe mumthunzi

Wake, tisachoke.

Iye adzatiteteza,

Tidalire mphamvu zake.

Yehova M’lungu wathu,

Ateteza olungama.

2. Kaya ambiri agwe

Pambali pa iwe,

Udzatetezeka ndi

Okhulupirika.

Sudzaopa ngati kuti

Ndiwe udzawonongedwe

Udzaziona izi,

Uli mumapiko ake.

3. M’lungu akuteteza

Ukamayesedwa.

Sudzafooka ayi

Chifukwa cha mantha.

Sudzaopa mkango, ndipo

Chinjokanso udzaponda.

Yehova m’pothawira,

Amatisamaliradi.

(Onaninso Sal. 97:10; 121:3, 5; Yes. 52:12.)