Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 73

Tizikondana Kwambiri Kuchokera Mumtima

Tizikondana Kwambiri Kuchokera Mumtima

(1 Petulo 1:22)

1. Tiyenera kukondana

Mochokeradi mumtima

Zimene zimapangitsa

Kuti tizikondwa.

Chikondi chili mumtima

Tifuna kuchisonyeza

Potero tidzatsanzira

Atate Yehova.

Mawu ndi ntchito zathu

Zisonyeze kukonda ’nzathu.

Osowa tithandize

N’zomwe tingakwanitse.

Tichitire’na ulemu

Pamene athedwa nzeru,

Ayi tisawanenetu.

Tidzakhulupirika,

Tidzagwirizanika.

2. Pamenetu tikondana

Sitikwiyirana msanga,

Tikhala osangalala,

Ndi kudalirana.

Tidzakhala ndi mabwenzi

Omwe tingadaliredi,

Ndi kumakondana zedi

Ndi kumasonkhana.

Tonse timalakwitsa

N’kulankhula mosaganiza,

Choncho ndikofunika

Chifundo kusonyeza.

Timafuna kudziwika

Monga anthu okondana.

Choncho M’lungu wakumwamba

Tidzamulemekeza,

Inde kumutsanzira.

(Onaninso 1 Pet. 2:17; 3:8; 4:8; 1 Yoh. 3:11.)