Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 41

Lambirani Yehova Muli Achinyamata

Lambirani Yehova Muli Achinyamata

(Mlaliki 12:1)

1. Anyamata ndi atsikananu,

Ndinu ofunika kwa Mulungu.

Iye amakukondani zedi

Kudzeratu mwa makolo anu.

2. Lemekezani makolo anu,

Ndipo musapikisane nawo.

M’kakondedwa ndi anthu ndi M’lungu,

Mudzakondwera ndi unyamata.

3. Kumbukira Mlengi mu’nyamata

Uzikonda cho’nadi kwambiri.

Ukadzipereka kwa Yehova,

Iye ndithudi adzakondwera.

(Onaninso Sal. 71:17; Maliro 3:27; Aef. 6:1-3.)