Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 70

“Muzitsimikizira Kuti Zinthu Zofunika Kwambiri Ndi Ziti”

“Muzitsimikizira Kuti Zinthu Zofunika Kwambiri Ndi Ziti”

(Afilipi 1:10)

1. Tifunikira kudziwa zinthu

Zomwe ndi zofunika.

Kuzindikira zinthu zimene

Tiyenera kuchita.

Uzidana ndi choipa,

Sangalatsa

Mtima wa Yehova. Zipemphera,

Ziphunzira.

Tichite zinthu zofunika.

2. Palibe chofunika kuposa

Kufalitsa uthenga.

Kufufuza nkhosa za

Atate wathu ndi kuzipeza.

Inde zimve, Tizidyetse.

Tisonyeze

Chikondi kwa anzathu adziwe,

Amasuke.

Kulalikira n’kofunika.

3. Tikachita zofunika

Tidzakhala otetezeka.

Tidzakhala n’chiyembekezo,

Mtendere wosaneneka.

Tidzakhala ndi mabwenzi

Achikondi.

Tidalitsidwa tikaphunzira,

Ndikudziwa,

N’kuchita zinthu zofunika.

(Onaninso Sal. 97:10; Mat. 22:37; Yoh. 21:15-17; Mac. 10:42.)