Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 75

Tili ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala

Tili ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala

(Mateyu 5:12)

1. Tili ndi zifukwa zambiri

Zakuti tisangalale.

Ndipo anthu m’mayiko onse

Akugwirizana nafe.

Chimwemwe chathu ndi chosatha

Mawu a M’lungu tidziwa.

Iwo amatisangalatsa

Tifuna kuwaphunzira.

Zotisangalatsa n’zambiri

Mumtimamu zikuyaka.

Tikakumana ndi mavuto

Yehova atithandiza.

(KOLASI)

Amatisangalatsadi

Yehova Mulungu wathu.

Iye n’ngwabwino ndi ntchito zake

N’zazikulu ndi zamphamvu.

2. Kumwamba, nyanja ndi dzikoli

N’zosangalatsa kuona.

Yehova analenga zonse,

Kwathu ndi kuyamikira.

Ntchito yochitira umboni

Ikupita patsogolo.

Ufumu ukulamulira

Ubweretsa madalitso.

Kusangalala kwamuyaya

Kwayandikira tsopano.

Zimene anatilonjeza

Tidzasangalala nazo.

(KOLASI)

Amatisangalatsadi

Yehova Mulungu wathu.

Iye n’ngwabwino ndi ntchito zake

N’zazikulu ndi zamphamvu.

(Onaninso Deut. 16:15; Yes. 12:6; Yoh. 15:11.)