Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 86

Akazi Okhulupirika Ndiponso Alongo Achikhristu

Akazi Okhulupirika Ndiponso Alongo Achikhristu

(Aroma 16:2)

1. Sara, Esitere, Rute ndi ena—

Onsewa ’nali akazi abwino.

Anali odzipereka kwa M’lungu.

Timawadziwa ndi mayina awo.

Panali ena sanatchulidwe,

Iwotu Yehova ankawakondanso.

2. Akaziwatu amatikumbutsa

Za makhalidwe amene tifuna

Monga ubwino ndi kulimba mtima.

Ndi zitsanzo zotilimbikitsadi.

Inu alongo owatsanzira

Utumiki wanu ndi wofunikadi.

3. Atsikana, achemwali, amayi

Mumagwira ntchito mofunitsitsa.

Mumagonjera, mumadzichepetsa.

Musaope Mulungu ali nanu.

Ndipo iye akulimbitseni,

Musatekeseke, m’peze mphoto yanu.

(Onaninso Afil. 4:3; 1 Tim. 2:9, 10; 1 Pet. 3:4, 5.)