Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 54

Tikhale ndi Chikhulupiriro

Tikhale ndi Chikhulupiriro

(Aheberi 10:38, 39)

1. Kale Mulungu ankalankhula

Kudzera mwa aneneri.

Lero kudzera mwa mwana wake

Akuti ‘lapanitu.’

(KOLASI)

Kodi chikhulupiriro chathu

N’cho’na ndi cha ntchito?

Chikakhala choterocho,

N’chimenedi chimasunga moyo.

2. Ife mokondwa timvera Yesu,

Tilalikira Ufumu.

Ndipo tilankhula mwaufulu,

Sitibisa cho’nadi.

(KOLASI)

Kodi chikhulupiriro chathu

N’cho’na ndi cha ntchito?

Chikakhala choterocho,

N’chimenedi chimasunga moyo.

3. Ndife olimba m’chikhulupiro,

Sitidzabwerera m’mbuyo.

Kaya adani atiukire,

Tidzapezabe moyo.

(KOLASI)

Kodi chikhulupiriro chathu

N’cho’na ndi cha ntchito?

Chikakhala choterocho,

N’chimenedi chimasunga moyo.

(Onaninso Aroma 10:10; Aef. 3:12; Aheb. 11:6; 1 Yoh. 5:4.)