Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 88

Ana Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu

Ana Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu

(Salimo 127:3-5)

1. Mwamuna ’kakhala bambo,

Mkazinso akakhala ndi mwana.

Afunika akumbukire,

Mwanayo siwawo okha.

Ndi mphatso yochoka kwa M’lungu

Amapatsa chikondi ndi moyo.

Amapatsanso malangizo

Othandizadi kwa makolo.

(KOLASI)

Mphatso yanu njopatulika

Ndipo muisamalire.

M’phunzitseni mwana cho’nadi

Choncho mungamuthandize.

2. Malamulo ’nse a M’lungu

Muziwasunga mumtima mwanu.

Muziphunzitsa ana anu,

Uwu ndi udindo wanu.

Muziwaphunzitsa poyenda,

Podzuka ndi pa nthawi yopuma.

Choncho iwo sadzaiwala

Adzakhala odalitsidwa.

(KOLASI)

Mphatso yanu njopatulika

Ndipo muisamalire.

M’phunzitseni mwana cho’nadi

Choncho mungamuthandize.

(Onaninso Deut. 6:6, 7; Aef. 6:4; 1 Tim. 4:16.)