Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 68

Pemphero la Munthu Wovutika

Pemphero la Munthu Wovutika

(Salimo 4:1)

1. Yehova ndapempha:

“Imvani pemphero langa.”

Zilonda zanga zakula

Sizipola msanga.

Kuvutika ndi maganizo

Kwandifoola.

Ndikomereni mtima

Mulungu wotonthoza.

(KOLASI)

Ndidzutseni. Ndichizeni

Nkhawa zanga zichotseni.

Pa mavuto n’thandizeni,

Yehova ndilimbitseni.

2. Ndikafo’ka

Mawu anu amanditonthoza

Kwambiri,

Moti sindingathe kufotokoza.

Ndidziwe kuti,

Chikondi chanu ndi chosatha

Ndiponso n’chachikulu

Kuposa mtima wanga.

(KOLASI)

Ndidzutseni. Ndichizeni

Nkhawa zanga zichotseni.

Pa mavuto n’thandizeni,

Yehova ndilimbitseni.

(Onaninso Sal. 42:6; 119:28; 2 Akor. 4:16; 1 Yoh. 3:20.)