Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 85

Mphoto Yaikulu Yochokera Kwa Yehova

Mphoto Yaikulu Yochokera Kwa Yehova

(Mateyu 19:29)

1. Yehova amadziwa anthu onse

Omwe amam’tumikira.

Amadziwa kuti pa nthawi zina

Zinthu zina ’mamanidwa.

Ngati mwasiya abale ndi nyumba

M’lungu akudziwa bwino.

Amatipatsa ’bale auzimu

Ndi moyo m’paradaiso.

(KOLASI)

Yehova wotonthoza aone

Ndiponso akupatseni mphoto.

Bisalani m’mapiko ake,

N’ngokhulupirika, Iye n’ngwabwino.

2. Mwina n’kusankha kwawo mwina ayi

Kuti ena sali m’banja.

Akamafuna Ufumu wa M’lungu

Iwo amadalitsidwa.

Amasungulumwatu nthawi zina,

Zimenezi tikudziwa.

Monga abale ndi alongo awo

Tikhale olimbikitsa.

(KOLASI)

Yehova wotonthoza aone

Ndiponso akupatseni mphoto.

Bisalani m’mapiko ake,

N’ngokhulupirika, Iye n’ngwabwino.

(Onaninso Ower. 11:38-40; Rute 2:12; Mat. 19:12.)