Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 108

Tamandani Yehova Chifukwa cha Ufumu Wake

Tamandani Yehova Chifukwa cha Ufumu Wake

(Chivumbulutso 21:2)

1. Yehova ’nadzoza Yesu

Kuti alamulire,

Kuti chifuniro cha M’lungu

Padzikoli chichitike.

(KOLASI)

Tamandani Yehova ndithu

Chifukwa cha Wodzozedwa

Inu nkhosa zokhulupirika

Zomvera malamulo.

Tamandani Wodzozedwayo,

Wolamula wakumwamba,

Amene adzayeretsa dzina

Loyera la Mulungu.

2. Abale a Yesu Khristu

Iwo ndi osankhika.

Adzalamulira ndi Yesu.

Dzikoli adzayeretsa.

(KOLASI)

Tamandani Yehova ndithu

Chifukwa cha Wodzozedwa

Inu nkhosa zokhulupirika

Zomvera malamulo.

Tamandani Wodzozedwayo,

Wolamula wakumwamba,

Amene adzayeretsa dzina

Loyera la Mulungu.

(Onaninso Miy. 29:4; Yes. 66:7, 8; Yoh. 10:4; Chiv. 5:9, 10.)