Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 127

Malo Odziwika ndi Dzina Lanu

Malo Odziwika ndi Dzina Lanu

(1 Mbiri 29:16)

1. Yehova kukumangirani

Nyumbayi ndi mwayi wathu.

Tikuipereka tsopano

Lidziwike dzina lanu.

Zimene tingakupatseni

Zinalitu kale zanu.

Luso, ntchito ndi chuma chathu

Timakupatsani inu.

(KOLASI)

Tikupereka malowa

Kuti mudziwikedi.

Tikupereka malowa

Chonde alandireni.

2. Tikulemekeza inuyo

Pokutamandani pano,

Landirani ulemerero

Tikamachuluka muno.

Malowa tikukupatsani

Tidzawasamalirabe.

Ndipo apereke umboni

Inde mpaka kalekale.

(KOLASI)

Tikupereka malowa

Kuti mudziwikedi.

Tikupereka malowa

Chonde alandireni.

(Onaninso 1 Maf. 8:18, 27; 1 Mbiri 29:11-14; Mac. 20:24.)