Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 129

Tigwire Mwamphamvu Chiyembekezo Chathu

Tigwire Mwamphamvu Chiyembekezo Chathu

(Aheberi 6:18, 19)

1. Anthu akhala akuyenda mumdima

Ndipo sanapindule kanthu n’komwe.

Zadziwika kuti anthu ochimwa

Kuvutika sangakuchotse.

(KOLASI)

Tiyeni tiimbe mokondwera

Poti Ufumu wa M’lungu wafika!

Yesu adzachotsadi zoipa,

Chiyembekezochi n’chonga nangula.

2. Uthenga womwe ukumveka ndi woti:

“Tsiku la Mulungu layandikira.”

Anthu ake sadzamvanso chisoni

M’lungu wathu timuimbira.

(KOLASI)

Tiyeni tiimbe mokondwera

Poti Ufumu wa M’lungu wafika!

Yesu adzachotsadi zoipa,

Chiyembekezochi n’chonga nangula.

(Onaninso Hab. 1:2, 3; Sal. 27:14; Yow. 2:1; Aroma 8:22.)