Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 122

Khamu la Abale

Khamu la Abale

(Chivumbulutso 7:9, 10)

1. Abale ambirimbiri,

Inde ochuluka,

Aliyense ndi mboni

Yokhulupirika.

Tilipodi ambiri,

Tikuchulukabe.

Tachokeratu ku mafuko

Ndi mitundu yonse.

2. Abale ambirimbiri,

Timalalikira

Uthenga wabwinodi

Kwa ofuna kumva.

Ngakhale tingatope,

Yesu atipatsa

Mpumulo ndi mphamvu zambiri.

Tidzasangalala.

3. Abale ambirimbiri,

Otetezedwadi,

Otumikira M’lungu

Padziko lapansi.

Tilipodi ambiri,

Timalalikira,

Timagwira ntchito ndi

M’lungu Pomutumikira.

(Onaninso Yes. 52:7; Mat. 11:29; Chiv. 7:15.)