Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 121

Tizilimbikitsana

Tizilimbikitsana

(Aheberi 10:24, 25)

1. Pomwe timalimbikitsana

Kutumikira Yehova

Timakhaladi okondana

Komanso ogwirizana.

Chikondi cha anthu a M’lungu

Chimatipatsadi mphamvu.

Kumene tingatetezeke

Ndi mkati mwa mpingo wathu.

2. Mawu ochoka kwa abale

A pa nthawi yoyenera

Ndi olimbikitsa kwambiri

Ndipo amatitonthoza.

Kugwirira ntchito limodzi

Ndithu ndikosangalatsa,

Timafuna kuthandizana

Ndi kumalimbikitsana.

3. Popeza tsiku la Yehova

Layandikira kwambiri

Ndikofunika tisaleke

Kusonkhanatu pamodzi.

Tikufuna kutumikira

Ndi abale kwamuyaya.

Choncho ndi njira yachikondi

Kuti tizithandizana.

(Onaninso Luka 22:32; Mac. 14:21, 22; Agal. 6:2; 1 Ates. 5:14.)