Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 78

Kuleza Mtima

Kuleza Mtima

(Agalatiya 5:22)

1. Yehova Mbuye wathu

Amakonda dzina lake.

Amafunitsitsadi

Kuti lisamanyozedwe.

Kwanthawi yaitali

Wakhala ’kupirira.

Iyetu sanatope

Amaleza mtima.

Anthu m’mitundu yonse

Amafuna ’pulumuke.

Kuleza kwake mtima

Sikudzapita pachabe.

2. Kuti tisapatuke

Tikhale oleza mtima.

Tidzapeza mtendere

N’kupewa kumangokwiya.

Pochita ndi anzathu

Tidzaona zabwino,

N’kukhala odziletsa

Ngakhale m’mavuto.

Kuleza mtima kwathu

Ndiko kudzatithandiza

Kutsanzira Mulungu

Amene tikumudziwa.

(Onaninso Eks. 34:14; Yes. 40:28; 1 Akor. 13:4, 7; 1 Tim. 2:4.)