Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 132

Tiimbire Yehova Chifukwa Wapambana

Tiimbire Yehova Chifukwa Wapambana

(Ekisodo 15:1)

1. Muimbireni Yehova M’lungu wokwezeka.

Anaponya m’nyanja Aigup’to onyada.

Tamandani Ya. Palibe wina womuposa.

Yehova ndi dzina lake. Ndi wopambana.

(KOLASI)

Yehova ndinu wokwezeka

Simunasinthe ndinube Mfumu.

Adani anu muwagonjetsa

N’kuyeretsa dzina lanu.

2. Mitundu yonse eti ikutsutsa Yehova.

Iwonongedwabe ngakhale ndi yamphamvu.

Posachedwapa isesedwa ndi Amagedo.

Idzadziwa kuti Yehova ndi Mulungu.

(KOLASI)

Yehova ndinu wokwezeka

Simunasinthe ndinube Mfumu.

Adani anu muwagonjetsa

N’kuyeretsa dzina lanu.

(Onaninso Sal. 2:2, 9; 92:8; Mal. 3:6; Chiv. 16:16.)