Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 105

Zakumwamba Zimalengeza Ulemerero wa Mulungu

Zakumwamba Zimalengeza Ulemerero wa Mulungu

(Salimo 19)

1. Kumwamba kumatamanda Yehova.

Ntchito za manja ’ke Timazionatu.

Nthawi zonse zimamutamanda,

Nyenyezi zimasonyeza Kuti ndi wamphamvu.

2. Malamulo a M’lungu ndi angwiro,

Zikumbutso zake Zimatetezadi.

Zigamulo zake n’zolondola.

Mawu ake n’ngolungama. N’ngokoma kwambiri.

3. Kuopa Mulungu ndi kwamuyaya.

Malamulo ake Aposa golide.

Iwotu amatitsogolera.

Dzina lake loyeralo Tililemekeze.

(Onaninso Sal. 111:9; 145:5; Chiv. 4:11)