Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 76

Yehova Ndi Mulungu Wamtendere

Yehova Ndi Mulungu Wamtendere

(Afilipi 4:9)

1. M’lungu wamtendere

M’tithandize tikhale

Ndi mtendere,

Makhalidwe abwino achuluke.

Malangizo anu,

Alowe mumtimamu.

Tikukupemphani

Mutipatse mtendere wanu.

2. Anthu m’dziko lonse

Akusowa mtendere.

Koma mtendere

Monga mvula muwazira ife.

Uchulukitseni

Ndipo tidalitseni.

Chifuniro chanu

Tikufuna tichidziwedi.

3. Mumatithandiza,

Mumatiunikira.

Mawu anu,

Mzimu wanu, zimatitsogolera.

Mtendere wangati

Mame ochulukadi.

Utitsitsimule,

Ukhazikitse mtima pansi.

(Onaninso Sal. 4:8; Afil. 4:6, 7; 1 Ates. 5:23.)