Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 94

Timasangalala Ndi Mphatso Iliyonse Imene Mulungu Amatipatsa

Timasangalala Ndi Mphatso Iliyonse Imene Mulungu Amatipatsa

(Yakobo 1:17)

1. Mphatso zangwiro,

Zabwino, zomwe timafuna

Zimachokera kwa M’lungu

Wathu wakumwamba.

Iyetu sanasinthepo

Ngakhale pang’ono.

Yehova amatipatsa

Kuunika ndi moyo.

2. Zonse za pa moyo wathu

Sitidera nkhawa.

Timadziwa n’ngwachikondi

Adzatisamala.

Sitiwonongera nthawi

Pa zosathandiza.

Zomwe M’lungu amatipatsa

Zimatikwanira.

3. Zapamwamba mudzikoli

Kwa M’lungu n’zachabe.

Tichite zinthu

Zimene zidzatithandize.

Chuma chosungitsa M’lungu

Ndi chotetezeka.

Timayamikira mphatso

Yokhala okhutira.

(Onaninso Yer. 45:5; Mat. 6:25-34; 1 Tim. 6:8; Aheb. 13:5.)