Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 128

Zochitika za Padzikoli Zikusintha

Zochitika za Padzikoli Zikusintha

(1 Akorinto 7:31)

1. Mulungu anapereka

Mwana wake mmodzi yekha

Kuti zikhale zotheka

Kudzapulumutsidwa.

(KOLASI)

Ngakhale dzikoli

likusintha

Mulungu adzadalitsa

Dzikoli ndi kumwamba.

2. Dzikolitu likudwala

Kuvutika ndi kofala

Koma tikusangalala

Ufumu unabadwa.

(KOLASI)

Ngakhale dzikoli

likusintha

Mulungu adzadalitsa

Dzikoli ndi kumwamba.

(Onaninso Sal. 115:15, 16; Aroma 5:15-17; 7:25; Chiv. 12:5.)