Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 62

Kodi Ndife Anthu a Ndani?

Kodi Ndife Anthu a Ndani?

(Aroma 14:8)

1. Iwe ndi wandani?

Umvera m’lungu uti?

Amene umam’gwadirayo,

Iye ndiye m’lungu wako.

Milungu iwiri

Sungaitumikire,

Sungalambire awiri onse,

Sungakhulupirike.

2. Iwe ndi wandani?

Umvera m’lungu uti?

Zilitu ndi iwe kusankha

Woona mwina wonama.

Kodi Kaisara

Udakamukondabe?

Kapena udzamvera Yehova

N’kuchita ntchito yake?

3. Ine ndi wandani?

Ndidzamvera Yehova.

Atate wanga wakumwamba

Ine ndidzam’sangalatsa.

Anandiwombola

Popatsa mwana wake,

Ndim’lambirabe, Ndi dzina lake

Ndililemekezabe.

(Onaninso Yos. 24:15; Sal. 116:14, 18; 2 Tim. 2:19.)