Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 58

Pemphero Langa Losonyeza Kudzipereka

Pemphero Langa Losonyeza Kudzipereka

(Mateyu 22:37)

1. Tengani mtima wanga

Cho’nadi uzikonda.

Maganizo tengani

Ndikutumikireni.

2. Manja anga tengani

Akutumikireni.

Tengani mawu anga,

Ndi’mbire Mfumu yanga.

3. Moyo wanga mu’tenge,

Zabwino ndizichite.

Yehova nditengeni,

Ndikusangalatseni.

(Onaninso Sal. 40:8; Yoh. 8:29; 2 Akor. 10:5.)