Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 124

Alandireni Bwino

Alandireni Bwino

(Machitidwe 17:7)

1. Yehova ndi M’lungu wopanda tsankho

Amapatsa onse zofuna zawo.

Amapatsa dzuwa

Ngakhalenso mvula

Amatisangalatsa mtima.

Osauka tikamawathandiza.

Mulungu wathu tidzamutsanzira,

Adzatidalitsa tikamachitira

Ena zinthu mokoma mtima.

2. Pothandiza ena sitingadziwe

Madalitso omwe tingalandire.

Angakhale anthu achilendo ndithu,

Tiwapatse zosowa zawo.

Monga Lidiya wa m’nthawi yakale,

Akabwera kwathu tiwalandire.

M’lungu amadziwa

onse om’tsanzira

Pochitira ena chifundo.

(Onaninso Mac. 16:14, 15; Aroma 12:13; 1 Tim. 3:2; Aheb. 13:2; 1 Pet. 4:9.)