Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 133

Bwerani kwa Mulungu Kuti Mupulumuke

Bwerani kwa Mulungu Kuti Mupulumuke

(Zefaniya 2:3)

1. Mitundu ya anthu

Ikutsutsadi Yesu.

Nthawi yawo yolamula

Yatha watero M’lungu.

Ufumu wayamba

Ndipo wakhazikika.

Adani onse apadziko

Khristu adzawaphwanya.

(KOLASI)

Bweranitu kwa Yehova

Kuti mudzapulumuke.

Mumudalire,

M’khulupirike,

Khalani kumbali yake.

Adzakupulumutsani

Ndi mphamvu zake.

2. Sankhani tsopano

Anthunu apadziko

Kumvera kaya kukana

Uthengawu wabwino.

Ngakhale mavuto

Tingakumane nawo

Yehova amasamalira

Tikapempha thandizo.

(KOLASI)

Bweranitu kwa Yehova

Kuti mudzapulumuke.

Mumudalire,

M’khulupirike,

Khalani kumbali yake.

Adzakupulumutsani

Ndi mphamvu zake.

(Onaninso 1 Sam. 2:9; Sal. 2:2, 3, 9; Miy. 2:8; Mat. 6:33.)