Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 69

Ndidziwitseni Njira Zanu

Ndidziwitseni Njira Zanu

(Salimo 25:4)

1. Yehova tasonkhanatu pamodzi

Pomvera kuitana kwanu.

Mawu anu ndi nyale m’njira yathu,

Amatiphunzitsa za inu.

(KOLASI)

Ndiphunzitseni njira zanuzo

Ndikhale womvera malamulo.

Ndiyendetseni m’njira yoona

Malamulo anu ndizikonda.

2. Nzeru zanu Yehova ndi zakuya,

Mfundo zanu n’zolimbikitsa.

Mawu anu adzakhala kosatha,

Timapezamo zodabwitsa.

(KOLASI)

Ndiphunzitseni njira zanuzo

Ndikhale womvera malamulo.

Ndiyendetseni m’njira yoona

Malamulo anu ndizikonda.

(Onaninso Eks. 33:13; Sal. 1:2; 119:27, 35, 73, 105.)