Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 57

Kusinkhasinkha kwa Mtima Wanga

Kusinkhasinkha kwa Mtima Wanga

(Salimo 19:14)

1. Zomwe ndimasinkhasinkha,

Zimene ndimaganiza,

Zikukondweretseni Ya

Kuti ndikhale wolimba.

Pamene ndili ndi nkhawa

N’kumalephera kugona

Ndisinkhesinkhe za inu,

Inde zinthu zoyenera.

2. Zilizonse zolungama,

Zofunika ndi zoona,

Ndikamaziganizira

Zindipezetse mtendere.

Nzeru zanu n’zofunika

Komanso ndi zochuluka.

Choncho ndizisinkhasinkha

Zonena zanu mwakhama.

(Onaninso Sal. 49:3; 63:6; 139:17, 23; Afil. 4:7, 8; 1 Tim. 4:15.)