Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 60

Mulungu Adzakupatsani Mphamvu

Mulungu Adzakupatsani Mphamvu

(1 Petulo 5:10)

1. Panali chifukwa chimene Mulungu

Anakupatsira choonadi

Anaona mtima wofuna kuchita

Zabwino zomukondweretsadi.

Unalonjeza kum’tumikira

Ndipo Iye anakuthandiza

(KOLASI)

Ndi magazi a Yesu Anakuwombola

Adzakulimbitsa adzakuteteza.

Adzakutsogolera ndi mzimu woyera

Adzakulimbitsa adzakuteteza.

2. Mulungu anapereka mwana wake

Amafunadi zikuyendere.

Ngati mwana wakeyo sanatimane

Kukulimbitsa sangalephere.

Chikondi chako sangaiwale

Sangasiye konse anthu ake.

(KOLASI)

Ndi magazi a Yesu Anakuwombola

Adzakulimbitsa adzakuteteza.

Adzakutsogolera ndi mzimu woyera

Adzakulimbitsa adzakuteteza.

(Onaninso Aroma 8:32; 14:8, 9; Aheb. 6:10; 1 Pet. 2:9.)