Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 130

Moyo Ndi Wodabwitsa

Moyo Ndi Wodabwitsa

(Salimo 36:9)

1. Makanda onse, ndiponso mvula,

Mbewu komanso kuwala kwa dzuwa—

Ndizodabwitsa, zonse ndi mphatso.

Zimatithandiza kukhala ndi moyo.

(KOLASI)

Choncho tichitenji ndi mphatso iyi?

Tikonde Mulungu yemwe anatipatsa.

Sitingaipeze mphatsoyi patokha,

Mphatsoyi ya moyo ndi yodabwitsadi.

2. Ena ’ngasiye kulimba mtima

N’kunena kuti: ‘Kuli bwino kufa.’

Koma ifeyo sitili choncho.

Timayamikira kukhala ndi moyo.

(KOLASI)

Choncho tichitenji ndi mphatso iyi?

Tikonde anzathu amene tili nawo.

Sitingaipeze mphatsoyi patokha,

Mphatsoyi ya moyo ndi yodabwitsadi.

(Onaninso Yobu 2:9; Sal. 34:12; Mlal. 8:15; Mat. 22:37-40; Aroma 6:23.)