Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 134

Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano

Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano

(Chivumbulutso 21:1-5)

1. Yerekeza iwe ndi’ne

M’dziko la tsopano tili tonse.

Ona mmene udzamvere,

Kukhala m’dziko la mtendere.

Oipa onse achoka.

M’lungu wathu sadzalephera

Kusintha zonse padziko lapansi.

Tidzamuimbira nyimbo tikumati:

(KOLASI)

“Yehova M’lungu mwachita bwino,

Zonse zakhalano zatsopano.

Tikuimba nyimbo mwachisangalalo.

Ndinudi woyenera ulemelero.”

2. Taganizira m’tsogolo,

Iwe ndi’ne m’dziko latsopano.

Sitidzamva ndi kuona

Zinthu zotichititsa mantha.

Mmene analonjezera

Zachitika, zonse zatheka.

Tsopano aku’kitsa omwalira,

Iwo ndi ife tidzamuyamikira:

(KOLASI)

“Yehova M’lungu mwachita bwino,

Zonse zakhalano zatsopano.

Tikuimba nyimbo mwachisangalalo.

Ndinudi woyenera ulemelero.”

(Onaninso Sal. 37:10, 11; Yes. 65:17; Yoh. 5:28; 2 Pet. 3:13.)