Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Wokondedwa Wolengeza Ufumu:

Tayerekezerani kuti inuyo ndinu mmodzi wa atumwi ndipo mwaimirira paphiri la Maolivi. Kenako Yesu akuonekera pakati panu. Ndipo atatsala pang’ono kupita kumwamba, iye akuti: “Mukadzalandira mzimu woyera, mudzakhala ndi mphamvu. Ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Kodi mukanachita chiyani?

N’kutheka kuti mukanachita mantha chifukwa cha kukula kwa ntchitoyo. Mwina mukanadzifunsa kuti, ‘Kodi tingakwanitse bwanji ntchito yochitira umboni “mpaka kumalekezero a dziko lapansi,” popeza ndife ophunzira ochepa chabe?’ Mwina mukanakumbukiranso zimene Yesu anachenjeza pa usiku wake womaliza. Iye anati: “Kapolo sangakhale wamkulu kuposa mbuye wake. Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani. Ngati asunga mawu anga, adzasunganso mawu anu. Koma adzakuchitirani zonsezi chifukwa cha dzina langa, chifukwa amene anandituma ine sakumudziwa.” (Yoh. 15:20, 21) Mukaganizira mawu amenewa, mungadzifunse kuti, ‘Kodi tingakwanitse bwanji kuchitira umboni mokwanira pamene anthu akutizunza ndiponso kutitsutsa?’

Masiku anonso timakhala ndi mafunso ngati amenewa. Monga Mboni za Yehova, ntchito yathu ndi yochitira umboni mokwanira “mpaka kumalekezero a dziko lapansi” kwa “anthu a mitundu yonse.” (Mat. 28:19, 20) Ndiye, kodi tingakwanitse bwanji kugwira ntchito imeneyi, makamaka tikaganizira zoti Yesu ananeneratu kuti tidzatsutsidwa?

Buku la Machitidwe a Atumwi limatiuza nkhani yosangalatsa yonena za mmene atumwi ndiponso Akhristu anzawo oyambirira anakwanitsira kugwira ntchito imeneyi mothandizidwa ndi Yehova. Buku limene mukuwerengali lakonzedwa kuti likuthandizeni kuphunzira nkhani yosangalatsa kwambiri imeneyi. Muchita chidwi kwambiri mukaona kufanana kumene kulipo pakati pa atumiki a Mulungu a m’nthawi ya atumwi ndi atumiki ake masiku ano. Muonanso kuti kufananaku sikukhudza ntchito yolalikira yokha komanso dongosolo limene timatsatira pogwira ntchitoyo. Sitikukayikira kuti mukaona kufanana kumeneku, mulimbitsa chikhulupiriro chanu choti Yehova Mulungu akupitiriza kutsogolera mbali ya padziko lapansi ya gulu lake.

Tikukupemphererani ndipo tikukhulupirira kuti mukamaphunzira buku la Machitidwe, mukhala ndi chikhulupiriro cholimba chakuti Yehova adzakuthandizani ndi mphamvu yake ya mzimu woyera. Choncho, bukuli likulimbikitseni kupitiriza ‘kuchitira umboni mokwanira za Ufumu wa Mulungu’ ndi kuthandiza ena kuti amudziwe Yehova n’kukhala ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha.​—Mac. 28:23; 1 Tim. 4:16.

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova