GAWO 1

Mlengi Anapatsa Anthu Paradaiso

Mlengi Anapatsa Anthu Paradaiso

Mulungu analenga zinthu za mlengalenga komanso zonse za moyo padziko lapansi. Analenga anthu angwiro, mwamuna ndi mkazi ndi kuwaika m’munda wokongola ndipo anawapatsa malamulo oti azitsatira

ANTHU amati mawu otsatirawa ndi otchuka kwambiri pa mawu onse oyambira nkhani amene analembedwapo. Mawu ake ndi akuti: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Baibulo likuyamba kutiuza za Yehova Mulungu wamphamvuyonse, yemwe ndi wofunika kwambiri kuposa aliyense wotchulidwa m’Malemba Opatulika pogwiritsa ntchito mawu amenewa, omwe ndi amphamvu komanso osavuta kumva. Vesi loyambali likusonyeza kuti Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse za kumwamba ndi padziko lapansi. Mavesi otsatira akufotokoza kuti kwa zaka zambirimbiri, Mulungu anakonza dziko lapansili kuti tizikhalamo, ndipo analenga zinthu zonse zochititsa chidwi zimene timaziona.

Pa zinthu zonse zimene Mulungu analenga padziko lapansi, munthu ndi wofunika kwambiri. Mulungu analenga munthu m’chifaniziro chake, ndipo amatha kusonyeza makhalidwe a Yehova monga chikondi ndi nzeru. Mulungu anapanga munthu kuchokera m’dothi lapansi ndipo anam’patsa dzina lakuti Adamu, kenako anamuika m’paradaiso m’munda wa Edeni. Mulungu ndi amene anakonza munda umenewo, ndipo anadzalamo mitengo yambiri ya zipatso imene inalinso yokongola.

Kenako Mulungu anaona kuti ndi bwino kuti mwamunayu amupangire mnzake. Choncho Mulungu anatenga nthiti ya Adamu n’kupanga mkazi, amene anam’pereka kwa Adamu kuti akhale mkazi wake ndipo iye anam’patsa dzina lakuti Hava. Adamu anasangalala kwambiri ndipo mwa ndakatulo ananena kuti: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga ndi mnofu wa mnofu wanga.” Ndiyeno Mulungu anafotokoza kuti: “Pa chifukwa chimenechi, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.”—Genesis 2:22-24; 3:20.

Mulungu anapatsa Adamu ndi Hava malamulo awiri. Choyamba, anawauza kuti alime ndi kusamalira dziko lapansi limene ankakhalamo ndiponso kuti adzazemo ana awo. Chachiwiri, anawauza kuti asadye “zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa,” mtengo umodzi wokha m’munda wonsewo. (Genesis 2:17) Mulungu anawauza kuti akadzadya chipatso cha mtengo umenewo adzafa. Popereka malamulo amenewa, Mulungu anapatsa mwamuna ndi mkazi oyambawo mpata wosonyeza kuti akuvomereza kuti iye ndi Wolamulira wawo. Komanso pomvera malamulo amenewa, iwo akanasonyeza kuti amakonda Mulungu ndiponso kumuyamikira. Iwo anali ndi zifukwa zomveka zovomerezera ulamuliro wake wabwinowo. Anthu angwirowo analibe chilema chilichonse, chifukwa Baibulo limati: “Mulungu anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.”—Genesis 1:31.

—Nkhaniyi yachokera m’buku la Genesis chaputala 1 ndi 2.