GAWO 13

Mafumu Abwino Ndiponso Oipa

Mafumu Abwino Ndiponso Oipa

Mtundu wa Isiraeli unagawanika. Kwa nthawi yaitali, iwo ankalamulidwa ndi mafumu ndipo ambiri mwa mafumu amenewo anali osakhulupirika. Kenako Ababulo anawononga Yerusalemu

MONGA mmene Yehova ananenera, mtundu wa Isiraeli unagawanika chifukwa choti Solomo anasiya kulambira koona. Rehobowamu, mwana wa Solomo amene anayamba kulamulira iye atamwalira, anali wankhanza kwambiri. Chifukwa cha zimenezi, mafuko 10 a Isiraeli anamugalukira ndipo anapanga ufumu wawo wakumpoto. Koma mafuko awiri anakhalabe okhulupirika kwa Rehobowamu, amene anali wa m’banja la chifumu la Davide ku Yerusalemu, ndipo anapanga ufumu wakum’mwera wa Yuda.

Maufumu onse awiri anali ndi mavuto ambiri makamaka chifukwa choti mafumu ake nthawi zambiri ankakhala osakhulupirika ndiponso osamvera. Koma ufumu wakumpoto wa Isiraeli unali ndi mavuto ochuluka zedi poyerekezera ndi ufumu wakum’mwera wa Yuda chifukwa chakuti mafumu onse ankalimbikitsa kulambira konyenga, kungoyambira ndi mfumu yake yoyamba. Ngakhale kuti aneneri ankachita zinthu zodabwitsa, monga Eliya ndi Elisa amene anaukitsa akufa, Aisiraeli anapitiriza kuchita zinthu zoipa. Chifukwa cha zimenezi, Mulungu analola kuti Asuri awononge ufumu wakumpoto wa Isiraeli.

Ufumu wa Yuda unakhala zaka zoposa 100 ufumu wa Isiraeli utawonongedwa, komabe pambuyo pake Mulungu analanganso ufumu umenewu. Mafumu ochepa chabe a Yuda ndi amene anayesetsa kutsogolera anthu awo kuti azilambira Yehova pomvera machenjezo amene Mulungu ankapereka kudzera mwa aneneri ake. Mwachitsanzo, Mfumu Yosiya anayamba kuyeretsa dera lonse la ufumu wa Yuda pochotsa kulambira konyenga ndi kukonzanso kachisi wa Yehova. Kenako anthu ena atapeza buku la Chilamulo chimene Mulungu anapereka kudzera mwa Mose, Yosiya anakhudzidwa kwambiri moti analimbikitsa kulambira koona.

Koma n’zomvetsa chisoni kuti mafumu amene anabwera pambuyo pa Yosiya anali oipa chifukwa sanatengere chitsanzo chake chabwino. Choncho, Yehova analola kuti Ababulo awononge ufumu wa Yuda pamodzi ndi kachisi wake ku Yerusalemu. Anthu amene sanawaphe, anawagwira n’kupita nawo ku ukapolo ku Babulo, ndipo Mulungu anali ataneneratu kuti iwo adzakhala zaka 70 ku ukapoloko. Dziko la Yuda linakhala labwinja kwa nthawi yonseyo, ndipo kenako monga mmene Mulungu analonjezera, Aisiraeli analoledwa kubwerera kudziko lawo.

Komabe, palibe mfumu ya m’banja la Davide imene inalamulira mpaka pa nthawi imene Mpulumutsi, yemwe ndi Mesiya wolonjezedwa anayamba kulamulira. Zochita za mafumu ambiri a m’banja la Davide ku Yerusalemu zinasonyeza kuti anthu opanda ungwiro si oyenera kulamulira, koma ndi Mesiya yekha amene ali woyeneradi kulamulira. Motero, Yehova anauza mfumu yomaliza ya m’banja la Davide kuti: “Vula chisoti chachifumu. . . . Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa wina aliyense kufikira atabwera amene ali woyenerera mwalamulo kuutenga, ndipo ndidzaupereka kwa iye.”—Ezekieli 21:26, 27.

—Nkhaniyi yachokera m’mabuku a 1 Mafumu; 2 Mafumu; komanso pa 2 Mbiri chaputala 10 mpaka chaputala 36 ndi pa Yeremiya 25:8-11.