GAWO 14

Mulungu Ankalankhula Kudzera mwa Aneneri Ake

Mulungu Ankalankhula Kudzera mwa Aneneri Ake

Yehova ankasankha aneneri kuti azipereka uthenga wokhudza chiweruzo, kulambira koyera komanso wokhudza Mesiya amene anthu ankamuyembekezera

M’NTHAWI ya mafumu ku Isiraeli ndi ku Yuda, panali anthu ena apadera otchedwa aneneri. Anthu amenewa anali olimba mtima komanso anali ndi chikhulupiriro cholimba ndipo ankapereka uthenga wochokera kwa Mulungu. Tiyeni tione mfundo zinayi zikuluzikulu zofunika kwambiri zimene aneneri a Mulungu analosera.

1. Kuwonongedwa kwa Yerusalemu. Kale kwambiri aneneri a Mulungu, makamaka Yesaya ndi Yeremiya, anayamba kuchenjeza anthu kuti Yerusalemu adzawonongedwa ndipo adzakhala bwinja. Iwo anafotokoza momveka bwino chifukwa chake Mulungu anakwiya ndi zochita za anthu a mumzindawo. Anthu okhala mu Yerusalemu ankanena kuti akulambira Yehova, koma zinali zabodza chifukwa iwo ankachita zinthu zokhudzana ndi kulambira konyenga, ankachita ziphuphu komanso zachiwawa.—2 Mafumu 21:10-15; Yesaya 3:1-8, 16-26; Yeremiya 2:1–3:13.

2. Kubwezeretsa kulambira koyera. Anthu a Mulungu anamasulidwa mu ukapolo ku Babulo patapita zaka 70. Iwo anabwerera kudziko la kwawo limene linali la bwinja n’kukamanganso kachisi wa Yehova ku Yerusalemu. (Yeremiya 46:27; Amosi 9:13-15) Kuli zaka pafupifupi 200 zimenezi zisanachitike, Yesaya ananeneratu kuti Koresi ndi amene adzagonjetse mzinda wa Babulo n’kulola anthu a Mulungu kuti abwerere kwawo ndi kukabwezeretsa kulambira koyera. Yesaya anafotokozanso mwatsatanetsatane njira yapadera imene Koresi adzamenyere nkhondo pogonjetsa mzindawo.—Yesaya 44:24–45:3.

3. Kubwera kwa Mesiya komanso zimene zidzamuchitikire. Ulosi unaneneratu kuti Mesiya adzabadwira mumzinda wa Betelehemu. (Mika 5:2) Iye adzakhala wodzichepetsa ndipo adzafika mu Yerusalemu atakwera bulu. (Zekariya 9:9) Ngakhale kuti iye adzakhala wofatsa ndiponso wachifundo, anthu ambiri adzadana naye komanso adzamukana. (Yesaya 42:1-3; 53:1, 3) Kenako iye adzaphedwa mwankhanza kwambiri. Koma kodi iye akadzaphedwa ndiye kuti zonse zidzathera pomwepo? Ayi, chifukwa chakuti nsembe yake idzachititsa kuti anthu ambiri akhululukidwe machimo awo. (Yesaya 53:4, 5, 9-12) Ndipotu kuti zimenezi zitheke, iye anayenera kuukitsidwa.

4. Mesiya adzalamulira anthu padziko lapansi. Anthu opanda ungwiro amalephera kudzilamulira okha mwamtendere, koma Mesiya yemwenso ndi Mfumu adzatchedwa Kalonga Wamtendere. (Yesaya 9:6, 7; Yeremiya 10:23) Mu ulamuliro wake, anthu adzakhala pamtendere ndi anthu anzawo ngakhalenso ndi nyama. (Yesaya 11:3-7) Ndipo sikudzakhalanso matenda. (Yesaya 33:24) Pa nthawiyo ngakhale imfa idzatheratu. (Yesaya 25:8) Mu ulamuliro wa Mesiya, anthu amene anamwalira adzaukitsidwa kuti akhalenso ndi moyo padziko lapansi.—Danieli 12:13.

—Nkhaniyi yachokera m’mabuku a Yesaya, Yeremiya, Danieli, Amosi, Mika ndiponso Zekariya.