Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GAWO 20

Yesu Khristu Anaphedwa

Yesu Khristu Anaphedwa

Yesu anayambitsa mwambo watsopano, anaperekedwa ndipo anamukhomera pamtengo wozunzikirapo

YESU atagwira ntchito yolalikira kwa zaka zitatu ndi hafu, anadziwa kuti nthawi yoti akhale padziko lapansi yatsala pang’ono kutha. Atsogoleri achipembedzo chachiyuda anakonza chiwembu choti amuphe, koma ankaopa kuti anthu amene ankakhulupirira kuti Yesu ndi mneneri awaukira. Kenako Satana anachititsa Yudasi Isikariyoti amene anali mmodzi mwa ophunzira 12 a Yesu kuti amupereke kwa adani ake. Atsogoleri achipembedzowo anapatsa Yudasi ndalama 30 zasiliva kuti apereke Yesu.

Pa usiku womaliza wa moyo wake, Yesu anasonkhanitsa atumwi ake kuti achite nawo mwambo wa Pasika. Atatulutsa Yudasi m’chipinda chimene ankachitira mwambowo, Yesu anayambitsa mwambo watsopano wotchedwa Mgonero wa Ambuye. Iye anatenga mtanda wa mkate ndipo atapemphera anaupereka kwa atumwi 11 otsalawo. Iye ananena kuti: “Mkate uwu ukuimira thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi pondikumbukira.” Anachitanso chimodzimodzi ndi kapu ya vinyo. Iye anati: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano pamaziko a magazi anga.”—Luka 22:19, 20.

Usiku umenewo Yesu anali ndi zambiri zoti auze atumwi akewo. Iye anawapatsa lamulo latsopano lakuti azisonyezana chikondi chololera kuvutikira ena, ndipo anati: “Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yohane 13:34, 35) Iye anawalimbikitsa kuti asade nkhawa chifukwa cha mavuto oopsa amene anali pafupi kumuchitikira. Yesu anawapempherera mochokera pansi pa mtima, ndipo anaimba nawo nyimbo zotamanda Mulungu, kenako anapita kumunda wa Getsemane usiku womwewo.

M’munda wa Getsemane, Yesu anagwada pansi n’kupemphera mochokera pansi pa mtima. Kenako panafika gulu la asilikali, ansembe ndi anthu ena kuti adzamugwire. Ndiyeno Yudasi anafika pafupi n’kupsompsona Yesu kuti adaniwo amudziwe. Pamene asilikaliwo ankamanga Yesu, atumwi aja anathawa.

Kenako anthuwo anapita naye kubwalo lalikulu la milandu la Ayuda, ndipo kumeneko Yesu ananena kuti iye ndi Mwana wa Mulungu. Bwalo la milandulo linagamula kuti ali ndi mlandu wochitira Mulungu mwano ndipo anamuweruza kuti ayenera kuphedwa. Kenako anthuwo anatenga Yesu n’kupita naye kwa bwanamkubwa wachiroma dzina lake Pontiyo Pilato. Ngakhale kuti iye anaona kuti Yesu alibe mlandu uliwonse, anam’perekabe kwa khamu la anthu limene linkafuula kuti Yesu aphedwe.

Anthuwo anapita ndi Yesu ku Gologota, kumene asilikali achiroma anamukhomera pamtengo wozunzikirapo. Mozizwitsa, kunagwa mdima ngakhale kuti anali masana. Madzulo a tsiku lomwelo, Yesu anamwalira ndipo panachitika chivomerezi champhamvu. Mtembo wake anauika m’manda ochita kusema m’thanthwe. Tsiku lotsatira, ansembe anatseka mandawo n’kuikapo asilikali olondera. Koma Yesu sanakhale m’mandamo mpaka kalekale chifukwa panachitika chozizwitsa china chachikulu kwambiri.

—Nkhaniyi yachokera pa Mateyu chaputala 26 ndi 27, Maliko chaputala 14 ndi 15, Luka chaputala 22 ndi 23 komanso pa Yohane chaputala 12 mpaka 19.

^ ndime 15 Kuti mumve zambiri zokhudza kufunika kwa imfa ya Yesu, onani buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa masamba 47 mpaka 56.