Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zamoyo Zinasinthadi Kuchokera ku Zinthu Zina?​—Zimene Anthu Amanena Komanso Zoona Zake

Kodi Zamoyo Zinasinthadi Kuchokera ku Zinthu Zina?​—Zimene Anthu Amanena Komanso Zoona Zake

Wasayansi wotchuka kwambiri dzina lake Richard Dawkins ananena kuti: “Mfundo yoti zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina ndi yoona mofanana ndi mfundo yoti dzuwa limatentha.”16 Koma umboni woti dzuwa limatentha umaoneka ndipo asayansi atsimikizira zimenezi. Koma kodi pali umboni wotsimikizira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina?

Tisanakambirane yankho la funsoli, tiyeni tikambirane kaye nkhani ina yofunika. Asayansi azindikira kuti nthawi ikamapita, zamoyo zimatha kusintha pang’ono. Mwachitsanzo, anthu oweta agalu akhoza kusankha galu wamwamuna ndi wamkazi oti abereke ana n’cholinga choti anawo adzakhale ndi miyendo ifupiifupi kapena ubweya wautali kusiyana ndi makolo awo. *

Koma asayansi ena amanena kuti kusintha kwapang’onopang’ono ngati kumeneku, pambuyo pa zaka mabiliyoni ambiri, kunachititsa kuti zinthu ngati nsomba zisinthe n’kukhala achule komanso anyani asinthe n’kukhala anthu.

Charles Darwin limodzi ndi buku lake lakuti Origin of Species

Mwachitsanzo, Charles Darwin ankaphunzitsa kuti kusintha pang’ono kwa zamoyo kumasonyeza kuti zamoyozo zikhozanso kusintha kwambiri ngakhale kuti anthu sanaonepo zimenezi.17 Iye ankakhulupirira kuti pambuyo pa nthawi yaitali kwambiri, zamoyo zazing’ono kwambiri “zinkasintha mwapang’onopang’ono” mpaka kukhala za mtundu wina ndipo mitundu inayo inkasinthanso.18

Anthu ambiri amaona kuti mfundo imeneyi ndi yomveka. Iwo amaganiza kuti, ‘Ngati zamoyo zimatha kusintha pang’ono ndiye kuti n’zotheka kusintha kwambiri patapita nthawi yaitali.’ * Koma anthu amakhulupirira zimenezi chifukwa cha mfundo zitatu zimene anthu ena amanena. Tiyeni tikambirane mfundozi.

Zimene anthu amanena: Ngati zamoyo zimatha kusintha pang’ono ndiye kuti zikhoza kusinthiratu n’kukhala za mtundu wina. Anthu amakhulupirira kuti popeza maselo a nyama ndi zomera amatha kusintha, n’zotheka kuti zinthuzo zisinthe kwambiri n’kupanga mitundu yatsopano.19

Kusintha kwa maselo kungachititse kuti maluwa azisintha pang’ono monga zilili ndi duwa lalikululi

Zoona zake: Pakatikati pa selo iliyonse pamakhala malangizo ochititsa kuti nyama kapena zomera zizioneka mogwirizana ndi mtundu wake. * Asayansi apeza kuti kusintha kwa maselo kukhoza kuchititsa kuti maonekedwe a nyama ndi zomera asinthe pang’ono. Koma kodi n’zoona kuti kusintha kwa maselowo kungachititse zinthu kusinthiratu n’kukhala za mtundu wina? Kodi anthu amene akhala akufufuza pa nkhani imeneyi kwa zaka zoposa 100 apeza zotani?

Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1930, asayansi anazindikira mfundo ina yatsopano. Poyamba, iwo ankaganiza kuti ngati zamoyo zimasintha kuti zigwirizane ndi dera linalake, ndiye kuti n’zotheka kuti mitundu ina yatsopano ipangike. Koma pa nthawiyi anayamba kuganiza kuti ngati anthu atachititsa kuti maselo a zinthu zina asinthe, akhoza kupanganso bwinobwino mitundu ina ya nyama kapena zomera. Wasayansi wina ku Germany dzina lake Wolf-Ekkehard Lönnig, * yemwe wakhala akuphunzira za kusintha kwa zomera kwa zaka pafupifupi 30, ananena kuti ‘asayansi ambiri ndiponso akatswiri pa nkhani yobereketsa zomera komanso zinyama ankayembekezera kuti akhoza kuchita zinthu zazikulu.’ Iye ananenanso kuti: “Asayansi ankaona kuti akhoza kupeza njira zatsopano zobereketsera zomera komanso zinyama. Ankaganiza kuti ngati atachititsa kuti maselo a zomera kapena zinyama asinthe mmene akufunira ndiyeno n’kubereketsa zinthuzo akhoza kupanga zomera ndi zinyama zabwino kwambiri.”20 Ndipo ena anafika poganiza kuti akhoza kupanga mitundu yatsopano.

Ntchentche zimene zasintha koma ndi ntchentchebe

Asayansi a ku United States, Asia ndi ku Europe anayamba kuchita kafukufuku amene ankaganiza kuti awathandiza kuti asinthe zamoyo kukhala za mtundu wina pa kanthawi kochepa. Kodi iwo anapeza zotani pambuyo pa zaka 40? Munthu wina amene anachita nawo kafukufukuyu dzina lake Peter von Sengbusch ananena kuti: “Tagwiritsa ntchito ndalama zambiri pa kafukufuku wofuna kusintha maselo a zinthu n’cholinga choti tipange mitundu yatsopano koma talephera.”21 Lönnig ananena kuti: “Pofika m’ma 1980, zinthu zimene asayansi apadziko lonse ankayembekezera zinalephereka. M’mayiko ambiri, asayansi anasiya kufufuza zambiri pa nkhani yosintha maselo n’kumabereketsa zinthu. Anachita zimenezi chifukwa chakuti akayesa kusintha zinthu, zambiri mwa zamoyo zosinthidwazo . . . zinkafa kapena kukhala zofooka kusiyana ndi zoyamba.” *

Koma pa zaka 100 zimene ankafufuza za kusintha maselo a zinthu komanso zaka 70 zimene ankayesetsa kusintha zinthu n’kuzibereketsa, asayansi apeza zinthu zina zowathandiza kumvetsa ngati zamoyo zingasinthedi n’kukhala za mitundu ina. Lönnig ataona zimene anapezazi anati: “Kusintha kwa maselo sikungachititse kuti [zomera kapena nyama] zisinthe n’kukhala za mtundu watsopano. Mfundo imeneyi ikugwirizana ndi zonse zimene asayansi apeza pa kafukufuku amene achita m’zaka za m’ma 1900 wokhudza kusintha maselo ndipo zikuonekeratu kuti sizingatheke kusintha zamoyo kuti zikhale za mtundu watsopano.”

Malinga ndi zimene takambiranazi, kodi n’zotheka kuti zamoyo zamtundu watsopano zipangike chifukwa cha kusintha kwa maselo? Palibe umboni woti zimenezi zingachitike. Zimene Lönnig anapeza pa kafukufuku wake zinamuchititsa kunena kuti: “Kusintha kwa zamoyo kuli ndi malire ake ndipo palibe chimene chingachititse kuti kusinthako kupitirire malirewo.”22

Ndiye taganiziraninso mfundo iyi. Ngati asayansi ophunzira kwambiri alephera kupanga mitundu yatsopano ya zamoyo posintha maselo, kodi zingatheke kuti zamoyozo zingosintha pazokha n’kupanga mitundu yatsopano? Ngati kafukufuku wasonyeza kuti kusintha kwa maselo sikungachititse kuti mitundu yatsopano ya zamoyo ipangike, kodi zinatheka bwanji kuti zamoyo zisinthe pazokha kuchokera ku zinthu zina?

Zimene anthu amanena: Zamoyo zimene zimasintha kuti zigwirizane ndi dera linalake zinasinthiratu n’kukhala za mtundu wina. Darwin ankakhulupirira kuti zamoyo zimene zinasintha kuti zigwirizane ndi dera linalake zinkapulumuka, pomwe zamoyo zimene sizinasinthe zinkafa patapita nthawi. Asayansi ena amaphunzitsa kuti pamene zamoyo zinkafalikira padziko lonse n’kukhala m’madera osiyanasiyana, zamoyo zokhazo zimene zinkatha kusintha n’kumagwirizana ndi deralo n’zimene zinkapulumuka. Asayansi ena amakhulupirira kuti zimenezi zinachititsa kuti patapita nthawi mitundu yatsopano ya zamoyo ipangike.

Zoona zake: Monga tanenera kale, kafukufuku anasonyeza kuti kusintha kwa maselo a zomera ndiponso zinyama sikungachititse kuti zinthuzo zisinthiretu n’kukhala mitundu yatsopano. Koma kodi asayansi amapereka umboni wotani wosonyeza kuti zinthu zikasintha kuti zigwirizane ndi dera linalake zimasinthanso n’kukhala za mtundu watsopano? Mu 1999, bungwe lina la ku United States (National Academy of Sciences) linatulutsa kabuku kamene kamafotokoza za “mitundu 13 ya mbalame yotchedwa finch imene Darwin ankaphunzira ali kuzilumba za Galápagos.”23

M’zaka za m’ma 1970, gulu lina lochita kafukufuku, lomwe Peter R. ndi B. Rosemary Grant a kuyunivesite ya Princeton ankatsogolera, linayamba kufufuza za mbalamezi. Anthuwa anapeza kuti patatha chaka chimodzi kuzilumbazi kuli chilala, mbalame zimene zinali ndi milomo italiitali n’zimene zinapulumuka kwambiri. Popeza kuti amasiyanitsa mitundu 13 ya mbalamezi poona kukula kwa milomo yake, anaganiza kuti zimene anaonazi zikupereka umboni wamphamvu. Kabukuko kananenanso kuti: “Peter ndi Rosemary Grant amaona kuti ngati chilala chitamachitika kuzilumbazi kamodzi pa zaka 10 zilizonse, ndiye kuti mtundu watsopano wa mbalamezo ukhoza kupangika patangopita zaka 200 zokha.”24

Koma kabukuko sikananene zoti m’zaka zotsatira pambuyo pa chilalacho mbalame zokhala ndi milomo ifupiifupi zinachulukanso kuposa zinazo. Ochita kafukufuku anapeza kuti mbalame zapachilumbazi zinkachuluka kapena kuchepa mogwirizana ndi nyengo ya pa nthawiyo. Chaka china mbalame zokhala ndi milomo italiitali zinachuluka koma chaka china zimene zinachuluka ndi mbalame zokhala ndi milomo ifupiifupi. Iwo anaonanso kuti mitundu yosiyana ya mbalamezi inkaswana n’kubereka ana amene ankakhala bwinobwino kuderali kuposa makolo awo. Anaganiza kuti mbalamezi zikapitiriza kuchita zimenezi mwina mitundu iwiriyi idzasintha n’kukhala mtundu umodzi.25

Mbalame zimene Darwin ankaphunzira zija zinasonyeza kuti zikhoza kungosintha pang’ono n’cholinga choti zigwirizane ndi dera linalake

Choncho, kodi tinganene kuti kusintha kwa zamoyo kuti zizigwirizana ndi dera linalake kumachititsa kuti mitundu yatsopano ipangike? Wasayansi wina dzina lake George Christopher Williams anayamba kukayikira ngati zimenezi zingachitike.26 Mu 1999, wasayansi winanso dzina lake Jeffrey H. Schwartz analemba kuti kusinthaku kumathandiza kuti zamoyozo zizikhala bwinobwino zinthu za m’deralo zikasintha, koma sikuchititsa kuti mitundu yatsopano ipangike.27

Zikuonekeratu kuti mbalame zimene Darwin ankaphunzira zija sizikusintha n’kukhala za mtundu watsopano. Mpaka pano mbalamezo sizinasinthe, zidakali za mtundu wotchedwa finch. Komanso popeza mbalame zamilomo ifupiifupi imatha kukwatirana ndi zamilomo italiitali, mwina asayansi analakwitsa ponena kuti ndi zamitundu yosiyana. Zimenezi zikusonyezanso kuti ngakhale mabungwe akuluakulu a sayansi nthawi zina akhoza kupereka umboni wongofuna kuti ugwirizane ndi maganizo awo.

Zimene anthu amanena: Zinthu zakufa zakale zimasonyeza kuti zamoyo zinachita kusintha. Kabuku kamene bungwe lija linatulutsa kamachititsa munthu kuganiza kuti zinthu zakufa zimene asayansi apeza zimapereka umboni wokwanira wakuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Kamati: “Papezeka zinthu zakufa zambiri zosonyeza kuti zamoyo zinkasintha, moti zimavuta kuzindikira kuti kusinthako kunachitika liti. Zinthu zakufazo zimasonyeza kuti nsomba zinkasintha pang’onopang’ono mpaka kukhala m’gulu la achule, achule ankasintha mpaka kukhala m’gulu la njoka, njoka zinkasintha n’kukhala m’gulu la nyama zikuluzikulu, nawonso anyani ankasintha.”28

Zoona zake: Zimene kabukuka kananena ndi zodabwitsa. Tikutero chifukwa cha zimene wasayansi wina dzina lake Niles Eldredge ananena. Ngakhale kuti iye amakhulupirira kwambiri zoti zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina, ananena kuti zinthu zakufa zimene asayansi apeza sizisonyeza kuti zamoyo zinkasintha pang’onopang’ono, m’malomwake zimasonyeza kuti “zamoyo zambiri zinakhala nthawi yaitali popanda kusintha chilichonse.” *29

Zinthu zakufa zimene asayansi apeza zimasonyeza kuti mitundu ikuluikulu ya zinyama inaoneka mwadzidzidzi ndipo sinasinthe n’kukhala mtundu wina

Pofika pano, asayansi apeza zinthu zakufa zikuluzikulu zokwana 200 miliyoni komanso zing’onozing’ono zokwana mabiliyoni ambiri. Ochita kafukufuku ambiri amagwirizana ndi mfundo yakuti zinthu zakufazi zimasonyeza kuti mitundu ikuluikulu ya nyama inapezeka mwadzidzidzi ndipo sinasinthe n’kukhala mtundu wina. Zimasonyezanso kuti mitundu ina ya nyama inangosowa mwadzidzidzi.

N’chifukwa Chiyani Anthu Amakhulupirira Kuti Zinthu Zinachita Kusintha?

Kodi n’chifukwa chiyani asayansi ambiri amanena kuti mfundo yakuti zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina ndi yosatsutsika? Wasayansi wina dzina lake Richard Lewontin analemba kuti asayansi ambiri amafuna kukhulupirira zimenezi chifukwa chakuti “anasankha kale kukhulupirira kuti zinthu zonse m’chilengedwechi, kuphatikizapo zamoyo, zinakhalapo zokha popanda kulengedwa ndi winawake.” Lewontin ananenanso kuti asayansi ambiri amakana ngakhale kuganizira zoti pangakhale winawake amene analenga zinthu. Amatero chifukwa safuna kuvomereza ngakhale pang’ono kuti kuli Mulungu.”30

Magazini ina inalemba mawu amene wasayansi wina dzina lake Rodney Stark ananena pa nkhaniyi, kuti: “Kwa zaka pafupifupi 200 anthu akhala akunena kuti ngati munthu akufuna kukhala wasayansi, sayenera kukhalanso wachipembedzo.” (Scientific American) Iye ananenanso kuti m’mayunivesite ochita kafukufuku wa sayansi “anthu achipembedzo sanena chilichonse chokhudza zimene amakhulupirira.”31

Munthu akamakhulupirira zimene asayansi amaphunzitsa pa nkhani yoti zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina, ndiye kuti pali mfundo zina zitatu zimene mwina sakuziganizira. Choyamba, nthawi zina asayansi amene sakhulupirira kuti kuli Mulungu amalola maganizo awowo kuwasokoneza pochita kafukufuku. Chachiwiri, sitinganene kuti kusintha kwa maselo komanso kusintha kwa zamoyo zina kuti zizigwirizana ndi dera linalake kunachititsa kuti mitundu yatsopano ya zamoyo ipangike. Zili choncho chifukwa kafukufuku amene wachitika kwa zaka zoposa 100 wasonyeza kuti kusintha kwa maselo sikunachititse kuti ngakhale mtundu umodzi watsopano upangike. Chachitatu, mfundo yakuti zamoyo zonse zinachita kusintha pang’onopang’ono kuchokera ku chinthu chimodzi ilibe umboni. Tikutero chifukwa chakuti zinthu zakufa zimene asayansi apeza zimasonyeza kuti mitundu ikuluikulu ya zomera komanso zinyama inapezeka mwadzidzidzi ndipo sinasinthe n’kukhala mitundu ina ngakhale patapita zaka zambirimbiri. Kodi munthu amene saganizira mfundo zitatuzi ndiye kuti amakhulupirira zinthu zoona kapena zabodza? Kunena zoona kukhulupirira kuti zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina n’kukhulupirira zinthu zopanda umboni.

^ ndime 3 Kusintha kwa ana a agaluwo nthawi zambiri kumachitika chifukwa chakuti maselo ena a agaluwo sanagwire ntchito yake. Mwachitsanzo, pali agalu enaake amene amakhala ndi miyendo ifupiifupi chifukwa choti minofu yawo yokhala pakati pa mafupa sikula bwinobwino.

^ ndime 6 M’buku la Genesis, mawu oti “mtundu” amatanthauza zambiri kusiyana ndi zimene asayansi amatanthauza akamanena kuti “mtundu.” Nthawi zambiri asayansi akanena kuti pali “mtundu watsopano wa nyama,” kwenikweni amakhala akunena za nyama ya mtundu womwe ulipo kale kungoti ikusiyana pang’ono ndi zinzake.

^ ndime 8 Asayansi apeza kuti muselo muli zinthu zingapo zimene zimachititsa kuti nyama kapena zomera zizioneka m’njira inayake.

^ ndime 9 Lönnig amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kulengedwa. Mawu ake amene tawalemba m’kabukuka akungosonyeza maganizo ake, osati a bungwe la Max Planck Institute for Plant Breeding Research, limene iye amagwirako ntchito.

^ ndime 10 Pochita kafukufukuyu, anapeza kuti zinthu zikasinthidwa zinali zosatheka kuti zinthuzo zizisinthabe. Pa zomera 100 zimene ankazisintha, chimodzi chokha n’chimene chinkasankhidwa kuti ayese kuchisinthanso. Pa zomwe zinasankhidwazo, anapezanso kuti chimodzi pa 100, n’chimene chikanatha kuyenda malonda. Koma sanakwanitse kupanga ngakhale mtundu umodzi watsopano wa zomera. Atayesa kuchita zimenezi ndi nyama, zotsatira zake zinali zoipa kwambiri kuyerekezera ndi zimene anapeza posintha zomera, moti anangosiya kuchita kafukufuku wa zinyamazo.

^ ndime 21 Ngakhale zinthu zakufa zochepa zimene asayansi amagwiritsa ntchito kuti apereke umboni wakuti zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina ndi zokayikitsa. Onani tsamba 22 mpaka 29 la kabuku kakuti Mmene Moyo Unayambira​—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri kolembedwa ndi Mboni za Yehova.