CHIGAWO 1
Kodi Mulungu Amalankhula Nafe Motani?
Mulungu amalankhula nafe kudzera m’Baibulo. 2 Timoteyo 3:16
Mulungu woona anathandiza anthu kuti alembe maganizo ake m’buku limodzi lopatulika. Buku limeneli ndi Baibulo. M’Baibulo muli zinthu zofunika kwambiri zimene Mulungu amafuna kuti muzidziwe.
Mulungu amadziwa zinthu zimene zingatithandize, ndipo iye ndi amene angatipatse nzeru. Choncho ife tingakhale anzeru tikamamvetsera zimene akunena.—Miyambo 1:5.
Mulungu amafuna kuti munthu aliyense padziko lapansi aziwerenga Baibulo. Ndipo masiku ano Baibulo likupezeka m’zinenero zambirimbiri.
Ngati mukufuna kumvera Mulungu, muyenera kuwerenga Baibulo ndi kulimvetsa bwino.
Padziko lonse, anthu akumvetsera zimene Mulungu akunena. Mateyu 28:19
Anthu a Mboni za Yehova angakuthandizeni kuti mulimvetse bwino Baibulo.
Padziko lonse lapansi, iwo amaphunzitsa choonadi chonena za Mulungu.
Maphunziro amenewa ndi aulere. Mungathe kuphunziranso za Mulungu ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova imene ikupezeka kwanuko.
Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi
ESSENTIAL BIBLE TEACHINGS
Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona?
Ngati Baibulo linachokeradi kwa Mulungu, ndiye kuti liyenera kukhala losiyana kwambiri ndi mabuku ena onse.
ESSENTIAL BIBLE TEACHINGS
Kodi Analemba Baibulo Ndi Ndani?
Ngati Baibulo linalembedwa ndi anthu, kodi n’zomveka kunena kuti ndi Mawu a Mulungu? Kodi m’Baibulo muli mawu a ndani?
MISONKHANO
Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani?
Onani mkati mwa Nyumba ya Ufumu kuti mudziwe zimene zimachitika.
ZOKHUDZA IFEYO
Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji?
A Mboni za Yehova padziko lonse lapansi amadziwika bwino chifukwa cha ntchito yawo yophunzitsa anthu Baibulo kwaulere. Onani mmene amaphunzitsira.
MABUKU
Kodi Baibulo Mumalikhulupirira?
Kodi Baibulo ndi buku la nzeru za anthu kapena ndi Mawu a Mulungu?
MVERANI MULUNGU KUTI MUDZAPEZE MOYO WOSATHA